Saturday, March 29, 2025

Mafumu a ku Nkhata-Bay apempha a Chakwera kuti alamulire kwa zaka zina zisanu

Must Read

Pamsonkhano wandale wa chipani cha Malawi Congress (MCP) omwe udachitika la Mulungu kum’mwera kwa boma la Nkhata Bay, mfumu Zilakoma yati chipanichi chidzalowanso m’boma pa chisankho cha pa 16 September motsogozedwa ndi mtsogoleri wake, Dr. Lazarus Chakwera.

Gogo Zilakoma ati izi ndi kamba ka utsogoleri wabwino wa a Chakwera omwe ati anaitanitsa mafumu onse m’bomali kunyumba kwawo kukadya ndikucheza nawo limodzi ngati mafumu omwe amagwira ntchito ndi boma la panthawiyo.

Nayo Senior Chief Malengamzoma yavomerezana ndi zomwe anena a Zilakoma kuti ngakhale mafumu ang’onoang’ono anapita nawo kunyumba yamtsogoleri wa dziko lino yemwe amaganizira umoyo wa mafumu choncho palibe chifukwa chomutaya.

Pothilira ndemanga, Senior Chief Fukamapiri yati singapezeke ku misonkhano ya zipani zina kupatula ku msonkhano wa chipani cha MCP.

- Advertisement -spot_img

LEAVE A REPLY

Please enter your comment!
Please enter your name here

- Advertisement -spot_img
Latest News

President Chakwera encourages youths to embrace hardworking spirit

Lilongwe, March 27, Mana: President Dr. Lazarus Chakwera has encouraged the country's youth to embrace a spirit of hard...
- Advertisement -spot_img

More Articles Like This

- Advertisement -spot_img