Saturday, July 27, 2024

Mkulu wakale wa Reserve Bank Dr Kabambe ayamikira Malemu Kasambara

Must Read

Mkulu wakale wa Bank ya Reserve a Dr. Dalitso Kabambe ayamikira malemu Ralph Kasambara kaamba kogwira ntchito yothandiza a Malawi mozipereka.

A Kasambara, omwe anali m’modzi mwa akadaulo pa nkhani ya zamalamulo m’dziko muno amwalira lachisanu ku Lilongwe.

“Malemu Ralph Kasambara anali kadaulo pa ntchito za malamulo komanso mmodzi mwa a Malawi yemwe anadzipeleka kwambiri pa ntchito zothandiza a Malawi ngati nduna ya boma komanso ngati Attorney General mzaka za mbuyomu,” a Kabambe analemba pa tsamba lawo la Facebook.

Iwo anawonjezera kuti; “Imfa yawo yandikhudza kwambiri monganso momwe yakhudzila a Malawi ambiri ndipo pemphero langa ndiloti Mulungu atonthoze banja lonse losiyidwa komanso anamalira onse munthawi yowawitsa kwambiri ngati imeneyi.”

La Mulungu, a Kabambe adali nawo pa mwambo wachisoni opelekeza thupi la malemu Ralph Kasambara kunyumba kwawo ku Nyambadwe komanso ku misa yomwe inachitikira ku St Montfort Parish ku CI mu mzinda wa Blantyre.

Malingana ndi a Kabambe, “A Ralph Kasambara anali munthu okonda dziko lake komanso olimbikira kwambiri popititsa patsogolo ntchito za malamulo komanso chilungamo mdziko muno,”

Thupi la a Kasambara lilowa m’manda lero Lolemba m’boma la Nkhatabay.

A Kabambe ndi katswiri wodziwika bwino mdziko muno ku nkhani ya za chuma.

- Advertisement -spot_img

LEAVE A REPLY

Please enter your comment!
Please enter your name here

- Advertisement -spot_img
Latest News

TNM gives Umthetho Festival K5M boost…Zulu nation King kaZwelithini coming

Lilongwe, July 25, 2024–In fostering cultural heritage and unity, TNM Plc, has contributed K5 million towards this year’s celebration...
- Advertisement -spot_img

More Articles Like This

- Advertisement -spot_img